Kasungu
Kasungu ndi Mzinda Boma la Kasungu omwe uli mchigawo cha pakati cha dziko la Malawi. Kasungu uli pa mtunda wa pafupifupi ma kilometa 130 ku mpoto cha ku madzulo kuchokela ku kapitolo la Malawi, Lilongwe, ndipo mtunda wa 35 cha ku m'mawa kwa Kasungu National Park.
Mbiri
[Sinthani | sintha gwero]Munda wina waukulu (farm) ndiye pomwe padabadwira pulezidenti woyamba wa dziko la Malawi.
Nyengo ndi Jogalafe
[Sinthani | sintha gwero]Kasungu ali pa kati pa dziko la Malawi, ndipo adagona pa mtunda okwana 1342 meters kuchoka pa mtunda wogona nyanja (sea level). Pa chifukwa ichi Kasungu ali ndi nyengo ya "warm tropical climate" ndipo nyengo ya mvula (chilimwe) yochoka m'miyezi ya Novembala/Disembala mpaka Malichi/Epulo. Nyengo ya dzuwa kuchoka mwezi wa Meyi mpaka mwezi wa Okutobala. Mvula yomwe imagwa ku Kasungu imafika pafupifupi 500mm - 1200mm pa chaka.
Demographics
[Sinthani | sintha gwero]Chaka | Chiwerengelo cha Anthu |
---|---|
1987 | 11,591 |
1998 | 26,137 |
2008 | 59,696 |
2009 | 60,000 (est) |
2010 | 80,000 (est) |
Chiyankhulo
[Sinthani | sintha gwero]Chichewa ndiye chilankhulo chomwe chimayankhulidwa kwambili ku Kasungu. Koma pakuti Kasungu anayandikana kwambili ndi Mzimba (komwe chiyankhulo chachikulu ndi Chitumbuka), kumayankhulidwanso Chitumbuka.
Kayendedwe
[Sinthani | sintha gwero]Njira yayikulu yofikira ku Kasungu ndi kudzela Msewu wa galimoto, tsono munthu atha kupita ku Kasungu pa basi, minibasi kapena galimoto la pulayiveti. Ma pulani ali mkatikati okuti Njanji ya Thileni idutse mpa mkati mweni mweni mwa mzindawu. Kamba ka mavuto a mafuta a galimoto omwe anavuta zedi mu chaka cha 2010, kunali kovuta zedi kuyenda mu mzindawu chifukwa mafuta a galimoto amasowa zedi. Kunali kofunika kuthila ku Lilongwe (ngakhale movutikila zedi) kuti munthu athe kuyenda mu Kasungu ndi kubwelela komwe wachokela mosavuta. Izi zidapangitsa kuti mafuta ogulitsidwa mwa chinyengo (black Market) achuluke, zomwe zidali zoyipa zedi. Koma mapulani aliopo omanga payipi yayikulu ya mafuta yochoka ku Tanzania ndiponso omanga ma tanki akulu zedi osungilamo mafuta. Izi zanenedwa ndi Boma la Malawi.
Malo achisangalalo ndi Osangalatsa
[Sinthani | sintha gwero]Chinthu chomwe chili chochititsa chidwi zede mu mzindawu ndi Kasungu National Park.